2 Corinthians 11:27 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidagwira ntchito zolemetsa, ndipo kaŵirikaŵiri sindidalaŵe tulo. Ndidamva njala ndi ludzu, kaŵirikaŵiri osaona chakudya, ndipo kusoŵa zovala ndi kuzizidwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
m'chivutitso ndi m'cholemetsa, m'madikiro kawirikawiri, m'njala ndi ludzu, m'masalo a chakudya kawirikawiri, m'chisanu ndi umaliseche.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndakhala ndikugwira ntchito molimbika ndipo kawirikawiri ndakhala ndikuchezera usiku wonse osagona. Ndakhala ndikumva njala ndi ludzu ndipo kawirikawiri ndakhala wopanda chakudya. Ndakhala ndi kuzizidwa ndi wosowa zovala.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
m'cibvutitso ndi m'colemetsa, m'madikiro kawiri kawiri, 2 m'njala ndi ludzu, m'masalo a cakudyakawiri kawiri, m'cisanu ndi umarisece.