2 Corinthians 11:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidadzitsitsa ndekha ineyo, kuti inu mukule. Ndidakulalikirani mwaulere Uthenga Wabwino wa Mulungu. Kodi ndiye kuti pakutero ndidalakwa?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kodi ndachimwa podzichepetsa ndekha, kuti inu mukakwezedwe, popeza ndinalalikira kwa inu Uthenga Wabwino wa Mulungu mwaufulu?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kodi linali tchimo kwa ine kudzichepetsa nʼcholinga chakuti ndikukwezeni pamene ndinkalalikira Uthenga Wabwino wa Mulungu kwa inu mwaulere?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kodi ndacimwa podzicepetsa ndekha, kuti inu mukakwezedwe, popeza ndinalalikira kwa inu Uthenga Wabwino wa Mulungu mwaufulu?