2 Corinthians 11:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo pamene ndinali kwanuko, nditasoŵa kanthu, sindidavute aliyense, pakuti abale ena ochokera ku Masedoniya adaandipatsa zonse zimene ndinkasoŵa. Pa zonse ndinkasamala kwambiri kuti ndisakhale ngati katundu wokulemerani, ndipo ndidzapitirirabe kutero.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo pakukhala nanu, ndi kusowa, sindinasaukitsa munthu aliyense; pakuti abale akuchokera ku Masedoniya, anakwaniritsa kusowa kwanga; ndipo m'zonse ndinachenjera ndekha, ndisalemetse inu, ndipo ndidzachenjerapo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo pamene ndinali pakati panu, nditasowa kanthu, sindinalemetse munthu aliyense, pakuti abale ena amene anachokera ku Makedoniya anandipatsa zonse zimene ndinkazisowa. Ndayesetsa kuti ndisakhale cholemetsa kwa inu mʼnjira ina iliyonse, ndipo ndidzapitiriza kutero.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo pakukhala nanu, ndi kusowa, sindinasaukitsa munthu ali yense; pakuti abale akucokera ku Makedoniya, anakwaniritsa kusowa kwanga; ndipo m'zonse ndinacenjera ndekha, ndisalemetse inu, ndipo ndidzacenjerapo.