2 Corinthians 12:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndasanduka wopusa, koma ndinu mwandichititsa zimenezi. Ndinu mukadayenera kundichitira umboni. Pakuti ngakhale sindili kanthu, atumwi anu apamwamba aja sandipambana pa kanthu kalikonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndakhala wopanda nzeru, mwandichititsa kutero; pakuti inu munayenera kundivomereza; pakuti sindiperewera ndi atumwi oposatu m'kanthu konse, ndingakhale ndili chabe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndadzisandutsa wopusa, koma inu mwandichititsa zimenezi. Ndinu amene munayenera kundichitira umboni. Ngakhale kuti sindine kanthu, koma sindine wochepetsetsa kwa “atumwi apamwamba” aja.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndakhala wopanda nzeru, mwandtcititsa kutero; pakuti inu nunayenera kundibvomereza; pacuti sindiperewera ndi atumwiopoiatu m'kanthu konse, ndingakhale adiri cabe.