2 Corinthians 12:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kodi nchiyani chimene ndidachitira mipingo ina, inu osakuchitirani, kupatula chokhachi chakuti sindidakhale ngati katundu wokulemetsani? Ndikhululukireni kulakwa kwangaku.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti kuli chiyani chimene munachepetsedwa nacho ndi Mipingo yotsala ina, ngati si ichi kuti ine ndekha sindinasaukitsa inu? Ndikhululukireni choipa ichi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kodi inu munaoneka ochepa motani ku mipingo ina, kupatula kuti sindinali cholemetsa kwa inu? Mundikhululukire cholakwa chimenechi!
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti kuli ciani cimene munacepetsedwa naco ndi Mipingo yotsala yina, agati, si ici kuti ine ndekha sindirasaukitsa inu? Ndikhululukireni oipa ici.