2 Corinthians 12:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Aka nkachitatu tsopano kukonzeka kuti ndibwere kwanuko, ndipo sindidzakhala ngati katundu wokulemetsani. Sindikufuna zinthu zanu, koma ndikufuna inuyo. Pakuti si udindo wa ana kusungira makolo ao chuma, koma ndi udindo wa makolo kusungira ana ao chuma.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Taonani, nthawi yachitatu iyi ndapukwa ine kudza kwa inu, ndipo sindidzakusaukitsani; pakuti sindifuna zanu, koma inu; pakuti ana sayenera kuunjikira atate ndi amai, koma atate ndi amai kuunjikira ana.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndakonzeka tsopano kudzakuyenderani kachitatu, ndipo sindidzakhala cholemetsa kwa inu chifukwa ndikungofuna inuyo osati zinthu zanu. Pakuti ana sasamalira makolo koma makolo ndiwo asamalira ana.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Taonani, nthawi yaitatu iyi ndapukwa ine kudza kwa nu, ndipo sindidzakusaukitsani; pakuti sindifuna zanu, koma inu; cakuti ana sayenera kuunjikira atate adi amai, koma atate ndi amai kumjikira ana.