2 Corinthians 12:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kunena za ine, ndidzakondwa kupereka zanga zonse, ndi kutaya ngakhale moyo wanga womwe chifukwa cha inu. Ine ndikamakukondani kwambiri chotere, kodi ndiye kuti inuyo muzingondikonda pang'ono?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndidzapereka ndi kuperekedwa konse chifukwa cha miyoyo yanu mokondweratu. Ngati ndikonda inu kochuluka koposa, kodi ndikondedwa kochepa?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Motero ndidzakondwera kukupatsani zanga zonse zimene ndili nazo ndi kudziperekanso ine mwini chifukwa cha inu. Kodi ine ndikamakukondani kwambiri chotere, inuyo mudzandikonda pangʼono?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndidzapereka ndi kuperekedwa konse cifucwa ca miyoyo yanu mokondweratu. Ngati ndikonda inu kocuruka koposa, kodi ndikondedwa kocepa?