2 Corinthians 12:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Momwemo tsono, mudzandivomereza kuti ine sindidakhale ngati katundu wokulemetsani. Koma kapena wina adzati popeza kuti ndine wochenjera, ndidakuchenjeretsani.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma kukhale kotero; ine sindinalemetsa inu; koma pokhala wochenjera ine, ndinakugwirani ndi chinyengo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ena mwa inu amavomereza kuti sindinali cholemetsa. Komabe ena amaganiza kuti ndine wochenjera, ndipo ndinakuchenjererani.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma kukhale kotero; ine sindinalemetsa inu; koma pokhala wocenjera ine, ndinakugwirani ndi cinyengo.