2 Corinthians 12:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidapempha Tito kuti apite, kenaka ndidatuma mbale wathu wina pamodzi naye. Kodi Titoyo adakuchenjererani? Kodi suja iye ndi ine tinkachita zonse ndi mtima umodzi? Suja tinkatsata njira imodzimodzi?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndinadandaulira Tito, ndipo ndinatuma mbaleyo naye. Kodi Tito anakuchenjererani kanthu? Sitinayendayenda naye Mzimu yemweyo kodi? Sitinatsata mapazi omwewo kodi?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndinamupempha Tito kuti abwere kwanuko ndipo ndinamutumiza pamodzi ndi mʼbale wathu. Kodi kapena Tito anakudyerani masuku pamutu? Kodi iye ndi ine sitinachite zinthu mofanana ndi Mzimu mmodzi yemweyo?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kodi Tito anakucenjererani kanthu? Sitinayendayenda naye Mzimu yemweyo kodi? Sitinatsata mapazi omwewo kodi?