2 Corinthians 12:19 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kapena mwakhala mukuganiza kuti tikuyesa kudziteteza pamaso panu. Iyai, koma pokhala pamaso pa Mulungu, timalankhula mwa Khristu, ndipo pa zonsezi, okondedwa anga, timangofuna kukulimbitsani mtima.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mumayesa tsopano lino kuti tilikuwiringula kwa inu. Tilankhula pamaso pa Mulungu mwa Khristu. Koma zonse, okondedwa, zili za kumangirira kwanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kodi mukuyesa kuti nthawi yonseyi takhala tikudzitchinjiriza tokha? Takhala tikuyankhula pamaso pa Mulungu monga anthu amene ali mwa Khristu; ndipo abwenzi okondedwa, chilichonse chimene timachita ndi chofuna kukulimbikitsani.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mumayesa tsopano Uno kuti tirikuwiringula kwa, inu. Tilankhula pamaso pa Mulungu mwa Kristu. Koma zonse, okondedwa, ziri za kumangirira kwanu.