2 Corinthians 12:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndikudziŵa mkhristu wina amene adaatengedwa mwadzidzidzi kupita Kumwambamwamba. Papita zaka khumi ndi zinai chichitikire cha zimenezi. Sindidziŵa ngati zidaachitika ali m'thupi kapena ali kunja kwa thupi. Akudziŵa ndi Mulungu zimenezi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndidziwa munthu wa mwa Khristu, zitapita zaka khumi ndi zinai (ngati m'thupi, sindidziwa; ngati kunja kwa thupi, sindidziwa; adziwa Mulungu), anakwatulidwa wotereyo kunka naye Kumwamba kwachitatu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndikudziwa munthu mwa Khristu amene zaka khumi ndi zinayi zapitazo anatengedwa kupita kumwamba kwachitatu. Sindikudziwa ngati zinachitika ali mʼthupi kapena ayi, zimenezo akudziwa ndi Mulungu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndidziwa munthu wa mwa Kristu, zitapita zaka khumi ndi zinai (ngati m'thupi, sindidziwa; ngati kunja kwa thupi, sindidziwa; adziwa Mulungu), anakwatulidwa wotereyo kunka naye Kumwamba kwacitatu.