2 Corinthians 12:20 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndikuwopa kuti ndikadzabwera kwanuko, mwina nkudzakupezani muli osiyana ndi m'mene ndikadafunira. Ndikuwopa kuti mwina inunso nkudzandipeza ine wosiyana ndi m'mene mukadafunira. Ndikuwopanso kuti mwina ine nkudzapeza kukangana, kaduka, kupsa mtima, kudzikonda, kusinjirirana, ugogodi, kudzitukumula, ndiponso chisokonezo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti ndiopa, kuti kaya, pakudza ine, sindidzakupezani inu otere onga ndifuna, ndipo ine ndidzapezedwa ndi inu wotere wonga simufuna; kuti kaya pangakhale chotetana, kaduka, mikwiyo, zilekanitso, maugogodi, ukazitape, zodzikuza, mapokoso;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti ndikuona kuti pamene ndibwera sindidzakupezani monga mmene ndikufunira kuti muzikhalira, ndipo simungadzandione monga mmene mukufunira kundionera. Ndikuopa kuti pangadzakhale mkangano, nsanje, kupserana mitima, kugawikana, ugogodi, miseche, kudzitukumula ndi chisokonezo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti ndiopa, kuti kaya, pakudza ine, sindidzakupezani inu otere onga ndifuna, ndipo ine ndidzapezedwa ndi inu wotere wonga simufuna; kuti kaya pangakhale cotetana, kaduka, mikwiyo, zilekanitso, maugogodi ukazitape, zodzikuza, mapokoso;