2 Corinthians 12:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndikadafuna kunyada, sindikadakhala ngati wopusa, chifukwa ndikadalankhula zoona zokha. Koma sindidzanyada, kuwopa kuti wina aliyense angandiyese wopambana, kusiyana ndi m'mene amandiwonera, ndiponso ndi m'mene amandimvera ndikamalankhula.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti ngati ndikafuna kudzitamandira, sindidzakhala wopanda nzeru; pakuti ndidzanena choonadi; koma ndileka, kuti wina angandiwerengere ine koposa kumene andiona ine, kapena amva za ine.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngakhale nditafuna kudzitamandira, sindingakhale chitsiru, chifukwa ndikunena zoona. Koma ndimapewa kuti pasapezeke munthu wondiganizira moposera chimene ndili chifukwa cha zimene ndimachita kapena kuyankhula,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti ngati ndikafuna kudzitamandira, sindidzakhala wopanda nzeru; pakuti ndidzanena coonadi; koma ndileka, kuti wina angandiwerengere ine koposa kumene andiona ine, kapena amva za ine.