2 Corinthians 12:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma kuwopa kuti ndingamadzitukumule chifukwa cha zazikulu kwambiri zimene Ambuye adandiwululira, Mulungu adandipatsa cholasa ngati minga m'thupi. Adalola wamthenga wa Satana kuti azindimenya, kuti ndingamanyade kwambiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kuti ndingakwezeke koposa, chifukwa cha ukulu woposa wa mavumbulutso, kunapatsidwa kwa ine munga m'thupi, ndiye mngelo wa Satana kuti anditundudze, kuti ndingakwezeke koposa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
kapena chifukwa cha mavumbulutso aakulu kuposa awa. Choncho, kuti ndisadzitukumule, ndinayikidwa minga mʼthupi langa, wamthenga wa Satana, kuti adzindizunza.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kuti ndingakwezeke koposa, cifukwa ca ukulu woposa wa mabvumbulutso, kunapatsidwa kwa ine munga m'thupi, ndiye mngelowa Satana kutianditundudze, kuti ndingakwezeke koposa.