2 Corinthians 13:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Aka nkachitatu tsopano kuti ndibwere kwanuko. Mau a Mulungu akuti, “Mlandu uliwonse uzitsimikizika ndi umboni wa anthu aŵiri kapena atatu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nthawi yachitatu iyi ndilinkudza kwa inu. Pakamwa pa mboni ziwiri kapena zitatu maneno onse adzakhazikika.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Uwu ndi ulendo wachitatu ndikubwera kudzakuyenderani. “Nkhani itsimikizike ndi umboni wa anthu awiri kapena atatu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nthawi yacitatu iyi ndirinkudza kwa inu. Pakamwa pa mboni ziwiri kapena zitatu maneno onse adzakhazikika.