2 Corinthians 13:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndikulemba zimenezi ndisanafike kwanu, kuti ndikadzafika, pasadzakhale chifukwa choti ndidzagwiritse ntchito ulamuliro wanga mwaukali. Ambuye adandipatsa ulamulirowo kuti ndilimbitse mpingo, osati kuti ndiupasule.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa cha ichi ndilembera izi pokhala palibe ine, kuti pokhala ndili pomwepo ndingachite mowawitsa, monga mwa ulamuliro umene Ambuye anandipatsa ine wakumangirira, ndipo si wakugwetsa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nʼchifukwa chake ndimalemba zinthu zoterezi pamene ndili kutali, kuti ndikabwera ndisadzagwiritse ntchito ulamuliro wanga mokalipa, uwu ndi ulamuliro umene Ambuye anandipatsa kuti ndikukuzeni inu osati kukuwonongani.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa ca ici ndilembera izi pokhala palibe ine, kuti pokhala ndiri pomwepo ndingacite mowawitsa, monga mwa ulamuliro umene Ambuye anandipatsa ine wakumangirira, ndipo si wakugwetsa.