2 Corinthians 13:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Inu amene mudaachimwa kale, ndiponso ena onse, paja ndidaakuuzani pamene ndinali kwanuko kachiŵiri kaja ndipo ndikubwereza kukuuziranitu tsopano ndisanafike, kuti ndikadzabweranso, sindidzamchitira chifundo wina aliyense.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndinanena kale, ndipo ndinena ndisanafikeko, monga pamene ndinali pomwepo kachiwiri kaja, pokhala ine palibe, kwa iwo adachimwa kale ndi kwa onse otsala, kuti, ngati ndidzanso sindidzawaleka;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndinakuchenjezani kale pamene ndinali nanu ulendo wachiwiri uja. Tsopano ndikubwereza ndisanafike. Ndikabweranso sindidzachitira chifundo amene anachimwa poyamba paja kapena wina aliyense amene anachimwa,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndinanena kale, ndipo ndinena ndisanafikeko, monga pamene ndinali pomwepo kaciwiri kaja, pokhala ine palibe, kwa iwo adacimwa kale ndi kwa onse otsala, kuti, ngati ndidzanso sindidzawaleka;