2 Corinthians 13:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anali wofooka pamene adapachikidwa pa mtanda, komabe tsopano ali moyo mwa mphamvu ya Mulungu. Ifenso ndife ofooka mwa Iye, koma tidzakhala amoyo pamodzi naye ndi mphamvu ya Mulungu, pogwira ntchito yathu pakati panu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
pakuti anapachikidwa m'ufooko, koma ali ndi moyo mu mphamvu ya Mulungu. Pakuti ifenso tili ofooka mwa Iye, koma tidzakhala ndi moyo pamodzi ndi Iye, mu mphamvu ya Mulungu, ya kwa inu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pofuna kutsimikizira, anapachikidwa ali wofowoka koma ali ndi moyo mwamphamvu ya Mulungu. Chomwechonso, ife ndife ofowoka mwa Iye, koma tidzakhala ndi moyo pamodzi naye ndi mphamvu ya Mulungu, potumikira pakati panu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
pakuti anapacikidwa m'ufoko, koma ali ndi moyo mu mphamvu ya Mulungu. Pakuti ifenso tiri ofok a mwa iye, koma tidzakhala ndi moyo pamodzi ndi iye, mu mphamvu ya Mulungu, ya kwa inu.