2 Corinthians 13:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tikupempha Mulungu kuti musachite choipa chilichonse. Osati kuti ife tiwoneke ngati opambana, koma kuti inu muchite zimene zili zoyenera, ngakhale ife tiwoneke ngati talephera.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo tipemphera Mulungu kuti musachite kanthu koipa; sikuti ife tikaoneke ovomerezeka, koma kuti inu mukachite chabwino, tingakhale ife tikhala monga osatsimikizidwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsopano tikupemphera kwa Mulungu kuti musadzachite kanthu kena kalikonse kolakwa. Osati chifukwa choti anthu aone kuti ife tapambana mayesowo koma kuti mudzachite zokhoza ngakhale anthu atamationa ngati olephera.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo tipemphera Mulungu kuti musacite kanthu koipa; sikuti ife tikaoneke obvomerezeka, koma kuti inu mukacite cabwino, tingakhale ife tikhala monga osatsimikizidwa.