2 Corinthians 2:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tithokoze Mulungu amene mwa Khristu amatitsogolera nthaŵi zonse m'kupambana kwake. Kudzera mwa ife Mulungu akupatsa anthu onse nzeru zodziŵira Khristu, ndipo nzeruzo zikuwanda ponseponse ngati fungo labwino.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma ayamikike Mulungu, amene atitsogolera m'chigonjetso mwa Khristu, namveketsa fungo la chidziwitso chake mwa ife pamalo ponse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma tithokoze Mulungu amene amatitsogolera nthawi zonse monga ogwidwa ku nkhondo a Khristu pa chipambano chake. Tsono amatigwiritsa ntchito yofalitsa ponseponse nzeru zodziwira Khristu ngati fungo labwino.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma ayamikike Mulungu, amene atitsogolera m'cigonjetso mwa Kristu, namveketsa pfungo la cidziwitso cace mwa ife pamalo ponse.