2 Corinthians 2:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nchifukwa chake ndidakulemberani kalata ija. Sindidafune kudza kwanuko, kuwopa kuti inuyo oyenera kundisangalatsanu mungandipweteketse mtima. Ndidaadziŵiratu kuti ine ndikamakondwa, nonsenunso mumakondwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndinalemba ichi chomwe, kuti pakudza ndisakhale nacho chisoni kwa iwo amene ayenera kukondweretsa ine; ndi kukhulupirira mwa inu nonse, kuti chimwemwe changa ndi chanu cha inu nonse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nʼchifukwa chake ndinakulemberani monga ndinachitiramo kuti nditabwera kwanuko ndisadzamve chisoni ndi anthu oyenera kundisangalatsa. Ndinali ndi chikhulupiriro ndi inu nonse kuti inuyo mukakhala ndi chimwemwe poona kuti inenso ndili ndi chimwemwe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndinalemba ici comwe, kuti pakudza ndisakhale naco cisoni kwa iwo amene ayenera kukondweretsa ine; ndi kukhulupirira mwa inu nonse, kuti cimwemwe canga ndi canu ca inu nonse.