2 Corinthians 2:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene ndidakulemberani kalata ija, mtima wanga unali wovutika ndi wopsinjika ndithu, ndipo ndinkalira misozi. Sindidafune kukupweteketsani mtima, koma makamaka ndinkafuna kuti mudziŵe kuti ndimakukondani kwambiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti m'chisautso chambiri ndi kuwawa mtima ndinalembera inu ndi misozi yambiri; si kuti ndikumvetseni chisoni, koma kuti mukadziwe chikondi cha kwa inu, chimene ndili nacho koposa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti ndinakulemberani kalata ija ndili wopsinjika ndi wowawidwa mtima kwambiri ndi kutuluka misozi yambiri, osati pofuna kukumvetsani chisoni koma kuti ndikudziwitseni kuti ndimakukondani kwambiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti m'cisautso cambiri ndi kuwawa mtima ndinalembera inu ndi misozi yambiri; si kuti ndikumvetseni cisoni, koma kuti mukadziwe cikondi ca kwa inu, cimene ndiri naco koposa.