2 Corinthians 3:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kodi ponena izi ndiye kuti tikuyamba kudzichitira umboni tokha? Kodi kapena nkofunika kuti ifenso, monga anthu ena, tikhale ndi makalata otichitira umboni kwa inu, kapena makalata aumboni ochokera kwa inu?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kodi tilikuyambanso kudzivomereza tokha? Kapena kodi tisowa, monga ena, akalata otivomerezetsa kwa inu, kapena ochokera kwa inu?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kodi tayambanso kudzichitira umboni tokha? Kapena kodi ifenso tikufuna makalata otivomereza kwa inu, kapena ochokera kwa inu monga anthu ena?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kodi tirikuyambanso kudzibvomereza tokha? kapena kodi tisowa, monga ena, akalata otibvomerezetsa kwa inu, kapena ocokera kwa inu?