2 Corinthians 3:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono ngati zinthu zosakhalitsa zidaafika ndi ulemerero, ndiye kuti zinthu zokhala mpaka muyaya zidzakhala ndi ulemerero wopambana.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti ngati chimene chilikuchotsedwa chinakhala m'ulemerero, makamaka kwambiri chotsalacho chili m'ulemerero.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo ngati zosakhalitsa zinabwera ndi ulemerero, koposa kotani ulemerero wamuyayawo!
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti ngati cimene cirikucotsedwa cinakhala m'ulemerero, makamaka kwambiri cotsalaco ciri m'ulemerero.