2 Corinthians 3:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma iwo nzeru zao zidauma, pakuti mpaka lero lino chophimba chomwe chija chimakhalapobe akamaŵerenga mabuku a m'Chipangano Chakale. Pajatu chophimbacho chimachotsedwa pokhapokha munthu akakhala mwa Khristu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
koma mitima yao inaumitsidwa; pakuti kufikira lero lomwe lino, pa kuwerenga kwa pangano lakale chophimba chomwechi chikhalabe chosavundukuka, chimene chilikuchotsedwa mwa Khristu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma nzeru zawo zinawumitsidwa, pakuti mpaka lero chophimbira chomwecho chikanalipo pamene akuwerenga Chipangano Chakale. Sichinachotsedwebe, chifukwa chimachotsedwa ngati munthuyo ali mwa Khristu yekha.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
koma mitima yao inaumitsidwa; pakuti kufikira lero lomwe lino, pa lcuwerenga kwa pangano lakale cophimba comweci cikhalabe cosabvundukuka, cimene cirikucotsedwa mwa Kristu.