2 Corinthians 3:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Malamulo ongolembedwa pa miyala aja adaperekedwa ndi ulemerero waukulu, kotero kuti Aisraele sankatha kuyang'anitsitsa nkhope ya Mose chifukwa cha kuŵala kwake. Komabe kuŵala kwakeko kunali kosakhalitsa. Tsono ngati malamulowo, amene ali odzetsa imfa, adaperekedwa ndi ulemerero wotere,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma ngati utumiki wa imfa wolembedwa ndi wolochedwa m'miyala, unakhala m'ulemerero, kotero kuti ana a Israele sanathe kuyang'anitsa pa nkhope yake ya Mose, chifukwa cha ulemerero wa nkhope yake, umene unalikuchotsedwa:
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma ngati utumiki umene unabweretsa imfa uja, wolembedwa ndi malemba pa mwalawu, unabwera ndi ulemerero mwakuti Aisraeli sanathe kuyangʼanitsitsa nkhope ya Mose chifukwa cha ulemerero wa pa nkhopeyo, ngakhale kuti unali kunka nuzilala,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Komangati utumiki wa imfa wolembedwa ndi wolocedwa m'miyala, unakhala m'ulemerero, kotero kuti ana a Israyeli sanathe kuyang'anitsa pankhope yace ya Mose, cifukwa ca ulemerero wa nkhope yace, umene unalikucotsedwa: