2 Corinthians 4:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Malembo akuti, “Ndidakhulupirira, nchifukwa chake ndidalankhula.” Tsono popeza kuti ife tili ndi mtima womwewo wokhulupirira, ifenso timalankhula.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma pokhala nao mzimu womwewo wa chikhulupiriro, monga mwa cholembedwacho, ndinakhulupirira, chifukwa chake ndinalankhula; ifenso tikhulupirira, chifukwa chake tilankhula;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kwalembedwa kuti, “Ndinakhulupirira; nʼchifukwa chake ndinayankhula.” Popeza ife tili ndi mtima womwewo wokhulupirira, ifenso timakhulupirira ndi kuyankhula,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma pokhala nao mzimu womwewo wa cikhulupiriro, monga mwa colembedwaco, ndinakhulupira, cifukwa cace ndinalankhula; ifenso tikhulupira, cifukwa cace tilankhula;