2 Corinthians 4:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Cholinga cha zonsezi nchakuti inu mupindule, ndipo kuti monga momwe anthu olandira madalitso a Mulungu akunka nachulukirachulukira, momwemonso othokoza Mulungu achulukirechulukire ndi kumchitira ulemu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti zonsezi nza kwa inu, kuti chisomocho, chochulukitsidwa mwa unyinjiwo, chichulukitsire chiyamiko ku ulemerero wa Mulungu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Zonsezi nʼkuti inu mupindule, kuti chisomochi chifikire anthu ochuluka kwambiri, amenenso adzathokoza mochuluka kwambiri ndi kupereka ulemerero kwa Mulungu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti zonsezi nza kwa inu, kuti cisomoco, cocurukitsidwa mwa unyinjiwo, cicurukitsire ciyamiko ku ulemerero wa Mulungu.