2 Corinthians 5:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Thupi limene timakhalamo pansi pano lili ngati msasa chabe. Koma tikudziŵa kuti msasawu ukadzapasuka, tidzakhala ndi nyumba ina imene Mulungu adatikonzera Kumwamba. Nyumbayo ndi yosamangidwa ndi manja a anthu, ndipo ndi yamuyaya.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti tidziwa kuti ngati nyumba ya pansi pano ya msasa wathu ipasuka, tili nacho chimango cha kwa Mulungu, ndiyo nyumba yosamangidwa ndi manja, yosatha, m'Mwamba.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Popeza tikudziwa kuti ngati msasa wa dziko lapansi umene tikukhalamo uwonongeka, tili ndi nyumba yochokera kwa Mulungu, nyumba yamuyaya yakumwamba, osati yomangidwa ndi manja a anthu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti tidziwa kuti ngati nyumba ya pansi pano ya msasa wathu ipasuka, tiri naco cimango ca kwa Mulungu, ndiyo nyumba yosamangidwa ndi manja, yosatha, m'Mwamba.