2 Corinthians 5:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pakuti tonsefe tiyenera kukaimirira poyera pamaso pa Khristu kuti atiweruze. Kumeneko aliyense adzalandira zomuyenerera, molingana ndi zimene adachita pansi pano, zabwino kapena zoipa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti ife tonse tiyenera kuonetsedwa kumpando wakuweruza wa Khristu, kuti yense alandire zochitika m'thupi, monga momwe anachita, kapena chabwino kapena choipa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti tonsefe tiyenera kukaonekera pa mpando woweruza wa Khristu, kuti aliyense wa ife akalandire zomuyenera molingana ndi zimene anachita ali mʼthupi; zabwino kapena zoyipa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti ife tonse tiyenera kuonetsedwa ku mpando wa kuweruza wa Kristu, kuti yense alandire zocitika m'thupi, monga momwe anacita, kapena cabwino kapena coipa.