2 Corinthians 5:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono popeza tikudziŵa kuti Ambuye ngoyenera kuŵaopa, timayesetsa kukopa anthu. Mulungu amatidziŵa kwathunthu, ndipo tikhulupirira kuti inunso mumatidziŵa kwenikweni m'mitima mwanu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Podziwa tsono kuopsa kwa Ambuye, tikopa anthu, koma tionetsedwa kwa Mulungu; ndipo ndiyembekezanso kuti tionetsedwa m'zikumbu mtima zanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono popeza tikudziwa tanthauzo la kuopa Ambuye, ife timayesetsa kukopa anthu. Mulungu amatidziwa bwino lomwe, ndipo tikukhulupirira kuti inunso mumatidziwa bwino mʼmitima mwanu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Podziwa tsono kuopsa kwa Ambuye, tikopa anthu, koma tionetsedwa kwa Mulungu; ndipo ndiyembekezanso kuti tionetsedwa m'zikumbu mtimazanu.