2 Corinthians 5:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Sitikuyesa kudzichitiranso umboni pamaso panu ai, koma tingofuna kukupatsani chifukwa choti muzitinyadira. Tikufuna kuti mukhale ndi kanthu koŵayankha amene angonyadira zooneka ndi maso, osati zamumtima.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Sitidzivomeretsanso ife tokha kwa inu, koma tikupatsani inu chifukwa cha kudzitamandira pa ife, kuti mukakhale nako kanthu kakutsutsana nao iwo akudzitamandira pooneka pokha, osati mumtima.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Sitikudzichitiranso tokha umboni kwa inu, koma tikukupatsani mwayi oti muzitinyadira. Tikufuna kuti muwayankhe amene amanyadira zinthu zooneka ndi maso osati zimene zili mu mtima.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Sitidzibvomeretsanso ife tokha kwa inu, koma tikupatsani inu cifukwa ca kudzitamandira pa ife, kuti mukakhale nako kanthu kakutsutsana nao iwo akudzitamandira pooneka pokha, osati mumtima.