2 Corinthians 5:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iye adafera anthu onse, kuti amene ali ndi moyo, asakhalenso ndi moyo wofuna kungodzikondweretsa okha, koma azikondweretsa Iye amene adaŵafera, nauka kwa akufa chifukwa cha iwowo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo adafera onse kuti iwo akukhala ndi moyo asakhalenso ndi moyo kwa iwo okha, koma mwa Iye amene adawafera iwo, nauka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Iye anafera anthu onse kuti amene ali ndi moyo, asakhale ndi moyo wofuna kudzikondweretsa okha, koma azikondweretsa amene anawafera naukitsidwa chifukwa cha iwowo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo adafera onse, kuti iwo akukhala ndi moyoasakhalenso ndi moyo kwa iwo okha, koma kwa iye amene adawafera iwo, nauka.