2 Corinthians 5:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nchifukwa chake kuyambira tsopano ife sitiganiziranso za munthu aliyense potsata nzeru za anthu chabe. Ngakhale kale tinkaganiza za Khristu potsata nzeru za anthu chabe, koma tsopano sitiganizanso za Iye motero.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kotero kuti ife sitidziwanso munthu tsopano monga mwa thupi; ndipo ngati tazindikira Khristu monga mwa thupi, koma tsopano sitimzindikiranso motero.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho, kuyambira tsopano mpaka mʼtsogolo ife sitiganizirapo za munthu aliyense monga mwanzeru za umunthu, ngakhale kuti poyamba tinkaganiza za Khristu mʼnjira imeneyi, koma tsopano sititeronso.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kotero kuti ife sitidziwanso munthu tsopano monga mwa thupi; ndipo ngati tazindikira Kristu monga mwa thupi, koma tsopano sitimzindikiranso motero.