2 Corinthians 5:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndiye kuti mwa Khristu Mulungu ankayanjanitsa anthu a pa dziko lonse lapansi ndi Iye mwini, osaŵaŵerengera machimo ao. Ndipo adatipatsa ifeyo mau onena za chiyanjanitsocho kuti tiŵalalike.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndiko kunena kuti Mulungu anali mwa Khristu, alinkuyanjanitsa dziko lapansi kwa Iye yekha, osawawerengera zolakwa zao; ndipo anaikiza kwa ife mau a chiyanjanitso.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mulungu ankayanjanitsa dziko lapansi kwa Iye mwini kudzera mwa Khristu, osawerengera anthu monga mwa zochimwa zawo. Ndipo watisungitsa ife uthenga uwu wa chiyanjanitso.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndiko kunena kuti Mulungu anali mwa Kristu, alinkuyanjanitsa dziko lapansi kwa Iyeyekha, osawawerengera zolakwa zao; ndipo anaikiza kwa ife mau a ciyanjanitso,