2 Corinthians 5:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ife amene tili mu msasa uno timalemedwa ndipo timabuula. Sitifuna kuuvula msasawu ai, koma kwenikweni tikadakonda kuvala nyumba ija ya Kumwamba pamwamba pake, kuti chimene chili chakufa chimizidwe ndi moyo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakutinso ife okhala mu msasawu tibuula, pothodwa; si kunena kuti tifuna kuvulidwa, koma kuvekedwa, kuti chaimfacho chimezedwe ndi moyo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamene tili mu msasa uno, timalemedwa ndipo timabuwula, chifukwa sitifuna kukhala amaliseche koma ovala nyumba yathu ya kumwamba, kuti chimene chili chakufa chimezedwe ndi moyo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakutinso ife okhala mu msasawu tibuula, pothodwa; si kunena kuti tifuna kubvulidwa, koma kubvekedwa, kuti caimfaco cimezedwe ndi moyo.