2 Corinthians 6:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Musamagwirizana ndi anthu akunja, monga ngati kuti iwo ndi inu mumafanana. Nanga kulungama kungagwirizane bwanji ndi kusalungama? Kapena kuŵala kungayanjane bwanji ndi mdima?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Musakhale omangidwa m'goli ndi osakhulupirira osiyana; pakuti chilungamo chigawana bwanji ndi chosalungama? Kapena kuunika kuyanjana bwanji ndi mdima?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Musamasenze goli pamodzi ndi osakhulupirira. Kodi pali mgwirizano wanji pakati pa kulungama ndi kusalungama? Kapena kodi pali mgwirizano wanji pakati pa kuwala ndi mdima?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Musakhale omangidwa m'goli ndi osakhulupira osiyana; pakuti cilungamo cigawanabwanji ndi cosalungama? Kapena kuunika kuyanjana bwanji nw mdima?