2 Corinthians 7:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono, inu okondedwa, popeza kuti tili ndi malonjezo ameneŵa, tiyeni tidzichotsere zinthu zonse zodetsa thupi lathu kapena mtima wathu. Ndipo pakuwopa Mulungu tiziyesetsa ndithu kukhala oyera mtima.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pokhala nao tsono malonjezano amenewa, okondedwa, tidzikonzere tokha kuleka chodetsa chonse cha thupi ndi cha mzimu, ndi kutsiriza chiyero m'kuopa Mulungu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Abwenzi okondedwa, popeza tili ndi malonjezo amenewa, tiyeni tidziyeretse, kusiyana nazo zilizonse zimene zikhoza kudetsa thupi ndi mzimu, ndipo tiyesetse kukhala oyera mtima poopa Mulungu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pokhala nao tsono malonjezano amenewa, okondedwa, tidzikonzere tokha kuleka codetsa conse ca thupi ndi ca mzimu, ndi kutsirfza ciyero m'kuopa Mulungu.