2 Corinthians 7:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Onani zimene chisoni chanu chokomera Mulungu chija chakuchitirani: chakupatsani changu chachikulu, chakukakamizani kwambiri kutsimikiza kuti simudalakwe, chakukwiyitsani kwambiri, ndipo chakuchititsani mantha aakulu. Chakulakalakitsani kuti mundiwone, ndipo chakupatsani changu chonditchinjiriza, ndiponso cholanga olakwa. Pa nkhani yonseyi umboni ulipo wakuti inu simudalakwepo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti, taonani, ichi chomwe, chakuti mudamvetsedwa chisoni cha kwa Mulungu, khama lalikulu lanji chidalichita mwa inu, komanso chodzikonza, komanso mkwiyo, komanso mantha, komanso kukhumbitsa komanso changu, komanso kubwezera chilango! M'zonse munadzitsimikizira nokha kuti muli oyera mtima m'menemo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Taonani zimene chisoni chimene Mulungu amafuna chatulutsa mwa inu. Chatulutsa khama lalikulu, chakuthandizani kuti mudzikonze nokha, chakukwiyitsani kwambiri, komanso chakupatsani mantha aakulu. Chakuchititsani kuti mufune kundiona ine, mwakhudzidwa kwambiri ndipo mukufuna kuonetsetsa kuti chilungamo chachitikadi. Pa nkhani yonseyi, mwaonetsadi kuti ndinu osalakwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti, taonani, ici comwe, cakuti mudamvetsedwa cisoni ca kwa Mulungu, khama lalikuru lanji cidalicita mwa inu, komanso codzikonza, komanso mkwiyo, komanso mantha, komanso kukhumbitsa komanso cangu, komanso kubwezera cilango! M'zonse muoadzitsimikizira nokha kuti muli oyera mtima m'menemo.