2 Corinthians 7:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Motero, ngakhale ndidakulemberani kalata imene ija, sindidailembe chifukwa cha amene adalakwa uja, kapena chifukwa cha amene iyeyo adamlakwira. Koma ndidailemba kuti ndikuwonetseni pamaso pa Mulungu kuti changu chanu chotitchinjiriza nchachikulu ndithu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake ndingakhale ndalembera kwa inu, sindinachita chifukwa cha iye amene anachita choipa, kapena chifukwa cha iye amene anachitidwa choipa, koma kuti khama lanu la kwa ife lionetsedwe kwa inu pamaso pa Mulungu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho ngakhale ndinakulemberani kalata ija, sindinayilembe ndi chifukwa cha amene analakwayo kapena wolakwiridwa, koma ndinayilemba kuti inuyo muone kudzipereka kwanu kwa ife pamaso a Mulungu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace ndingakhale ndalembera kwa inu, sindinacita cifukwa ca iye amene anacita coipa, kapena cifukwa ca iye amene anacitidwa coipa, koma kuti khama lanu la kwa ife lionetsedwe kwa inu pamaso pa Mulungu.