2 Corinthians 7:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zimenezi zatilimbitsa mtima kwambiri. Kuwonjezera pa zotilimbitsa mtimazo, chimwemwe cha Tito chidatikondweretsa kopambana, popeza kuti nonsenu mudamsangulutsa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa cha ichi tatonthozedwa; ndipo m'chitonthozo chathu tinakondwera koposa ndithu pa chimwemwe cha Tito, kuti mzimu wake unatsitsimutsidwa ndi inu nonse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Zimenezi zatilimbikitsa kwambiri. Kuwonjezera pa zotilimbikitsazo, tinakondwa kwambiri poona chisangalalo cha Tito, chifukwa nonsenu munamuthandiza kukhazikitsa mtima wake pansi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa ca icitatonthozedwa; ndipo m'citonthozo cathu tinakondwera koposa ndithu pa cimwemwe ca Tito, kuti mzimu wace unatsitsimutsidwa ndi inu nonse.