2 Corinthians 7:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidamuuzadi kuti ndimakunyadirani, ndipo inu simudandichititse manyazi. Koma monga momwe zonse zimene tidaakuuzani zinali zoona, momwemonso kudaoneka kuti zimene ndidauza Tito mokunyadirani, zinali zoona.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti ngati ndadzitamandira nako kanthu kwa iye chifukwa cha inu, sindinamvetsedwa manyazi; koma monga tinalankhula zonse ndi inu m'choonadi, koteronso kudzitamandira kwathu kumene kwa Tito, kunakhala choonadi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndinamuwuza kuti ndimakunyadirani, ndipo simunandichititse manyazi. Koma monga zonse zimene tinakuwuzani zinali zoona, tsono zomwe ndinawuza Tito zokunyadirani zinali zoona.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti ngati ndadzitamandira nako kanthu kwa iye cifukwa ca inu, sindinamvetsedwa manyazi; koma monga tinalankhula zonse ndi inu m'coonadi, koteronso kudzitamandira kwathu kumene kwa Tito, kunakhala coonadi.