2 Corinthians 7:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Makamaka chikondi chake pa inu nchachikulu kopambana pamene akumbukira kuti nonsenu mudamvera mau anga, ndipo mudamlandira ndi mantha ndi monjenjemerera.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo chikondi chenicheni chake chichulukira koposa kwa inu, pokumbukira kumvera kwanu kwa inu nonse, kuti munamlandira iye ndi mantha ndi kunthunthumira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo chikondi chake pa inu nʼchachikulu kwambiri akakumbukira kuti nonse munali omvera, munamulandira ndi mantha ndi kunjenjemera.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo cikondi ceni ceni care cicurukira koposa kwa inu, pokumbukira kumvera kwanu kwa inu nonse, kuti munamlandira iye ndi mantha ndi kunthunthumira.