2 Corinthians 7:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Sindikunena zimenezi kuti mupezeke olakwa. Paja monga ndanena kale, inu muli m'mitima mwathu ndithu, kotero kuti tili pamodzi, ngakhale tikhale moyo kapena timwalire.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Sindinena ichi kuti ndikutsutseni: pakuti ndanena kale kuti muli mu mitima yathu, kuti tife limodzi ndi kukhala ndi moyo limodzi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Sindikunena izi kuti mupezeke olakwa. Ndinanena kale kuti ife timakuganizirani kwambiri kotero kuti tili pamodzi, ngakhale tikhale moyo kapena timwalire.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Sindinena ici kuti ndikutsutseni: pakuti ndanena kale kuti muli mu mitima yathu, kuti tife limodzi ndi kukhala ndi moyo limodzi.