2 Corinthians 7:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndimakukhulupirirani kwambiri, ndipo ndimakunyadirani kwenikweni. Zondilimbitsa mtima zandichulukira, ndipo m'zovuta zathu zonse ndakondwa kopambana.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndilimbika mtima kwambiri pakunena nanu, kudzitamandira kwanga chifukwa cha inu nkwakukulu; ndidzazidwa nacho chitonthozo, ndisefukira nacho chimwemwe m'chisautso chathu chonse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndimakukhulupirirani kwambiri ndipo ndimakunyadirani kwambiri. Ndikulimbikitsidwa kwambiri; mʼmasautso athu onse, chimwemwe changa chilibe malire.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndilimbika mtima kwambiri pakunena nanu, kudzitamandira kwanga cifukwa ca inu nkwakukuru; ndidzazidwa naco citonthozo, ndisefukira naco cimwemwe m'cisautso cathu conse.