2 Corinthians 7:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ngakhale pamene tidafika ku Masedoniya sitidapeze mpumulo konse. Tidapeza zovuta ponseponse, popeza kuti panali kukangana ndi adani otizungulira, ndiponso mantha m'mitima mwathu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakutinso pakudza ife Masedoniya thupi lathu linalibe mpumulo, koma tinasautsidwa ife monsemo; kunjako zolimbana, m'katimo mantha.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti titafika ku Makedoniya, sitinapume nʼkomwe, koma tinavutitsidwa mbali zonse. Kunja kunali mikangano, ndipo mʼmitima mwathu munali mantha.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakutinso pakudza ife m'Makedoniya thupi lathu linalibe mpumulo, koma tinasautsidwa ife monsemo; kunjako zolimbana, m'katimo mantha.