2 Corinthians 7:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kalata yanga ija idakupwetekani mtima, komabe sindikuchita chisoni kuti ndidailemba. Ndidaachita chisoni poyamba, ndipo ndikuwona kuti kalatayo idakupwetekanidi mtima, ngakhale kanthaŵi pang'ono chabe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kuti ngakhale ndakumvetsani chisoni ndi kalata uja, sindiwawapo mtima, ndingakhale ndinawawa mtima; pakuti ndiona kuti kalata uja anakumvetsani chisoni, ngakhale kwa nthawi yokha.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngakhale kalata yanga ija inakupwetekani mtima, sindikudandaula kuti ndinalemberanji. Ngakhale zinandikhudza, ndikudziwa kuti kalata yanga inakupwetekani, koma kwa kanthawi kochepa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kuti ngakhale ndakumvetsani cisoni ndi kalata uja, sindiwawapo mtima, ndingakhale ndinawawa mtima; pakuti ndiona kuti kalata uja anakumvetsani cisoni, ngakhale kwa nthawi yokha.