2 Corinthians 7:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma tsopano ndakondwa, osati chifukwa ndidaakupwetekani mtima, koma chifukwa kuvutika kwanu kudakuthandizani kutembenuka mtima. Kuvutika kwanuko kunali kovomerezeka ndi Mulungu, motero sitidakutayitseni kanthu kabwino kalikonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tsopano ndikondwera, si kuti mwangomvedwa chisoni, koma kuti mwamvetsedwa chisoni ku kutembenuka mtima; pakuti munamvetsedwa chisoni cha kwa Mulungu, kuti tisakusowetseni m'kanthu kalikonse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma tsopano ndine wokondwa, osati chifukwa chakuti kalatayo inakupwetekani, koma chifukwa chakuti chisoni chanu chinakuthandizani kutembenuka mtima. Pakuti munamva chisoni monga mmene Mulungu amafunira, choncho simunapwetekedwe mwanjira iliyonse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tsopano ndikondwera, sikuti mwangomvedwa cisoni, koma kuti mwamvetsedwa cisoni ku kutembenuka mtima; pakuti munamvetsedwa cisoni ca kwa Mulungu, kuti tisakusowetseni m'kanthu kali konse.