2 Corinthians 8:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Malinga munthu akakhala ndi changu cha kupereka, Mulungu amalandira mokondwa zimene munthuyo ali nazo, ndipo samkakamiza kuti apereke zimene alibe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti ngati chivomerezocho chili pomwepo, munthu alandiridwa monga momwe ali nacho, si monga chimsowa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo ngati mtima ofunitsitsa ulipo, mphatsoyo imalandiridwa molingana ndi zimene munthuyo ali nazo, osati zimene alibe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti ngati cibvomerezoco ciri pomwepo, munthu alandiridwa monga momwe ali naco, si monga cimsowa.