2 Corinthians 8:23 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kunena za Tito, iyeyu ndi wantchito mnzanga amene amagwirizana nane pokuthandizani. Kunenanso za abale athu enawo, ngotumidwa ndi mipingo, ndipo Khristu amalemekezedwa chifukwa cha iwo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nanga za Tito, ali woyanjana wanga ndi wochita nane wa kwa inu; nanga abale athu, ali atumwi a Mipingo, ali ulemerero wa Khristu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kunena za Tito, ndiye mnzanga ndi wogwira naye ntchito pakati panu. Kunena za abale athu, ndiwo oyimirira mipingo ndi olemekezetsa Khristu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nanga za Tito, ali woyanjana wanga ndi wocita nane wa kwa inu; nanga abale athu, ali atumwi a Mipingo, ali ulemerero wa Kristu.